Tisiye Kuganiza Kuti Tilibe Kuthekera- Chilima

Wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Klaus Chilima wauza amalawi kuti asiye kuganiza kuti alibe kuthekela kopanga zinthu mwaukadaulo.

Bambo Chilima alankhula izi usiku wathawu pomwe amapelela uthenga wapadera mumzinda wa Lilongwe pakufunika kosintha kaganizidwe pofuna kutuluka dziko lino.

Malingana ndi a Chilima, nzika za dziko lino zisiye kuganiza kuti chabwino chilichonse oyenela kupanga ndi anzungu.

“Tikuyenela kudzilimbikitsa tokha kuti tidzinthe maganizidwe ndi kuchita chomwe tikufuna. Tisiye kuganiza kuti chilichonse chabwino ndichochokera kwa anzungu. Ifeso titha kuchita zinthu ena nkutengela,” adatelo A Chilima.

Wachiwiri wamtsogoleri wa dziko linoyi adati nzika za dziko lino ziri ndi kuthekera kosintha dziko zitasintha kaganizidwe.

“Ndi Kasinthidwe kamaganizidwe athu titha kusintha dziko lino kuchoka kuumphawi. Ena achita bwino zimenezi ndipo ifeso titha kutero,” adatero a Chilima.

Mtsogoleri wadziko liko a Lazarus Chakwera omwe adali mlendo olemekezeka pa mwambowu adayamikira a Chilima popeleka uthengawu wapadelawu pa mutu oti a Malawi akuyenera kusintha kaganizidwe.

A Chakwera adati mutu umene a Chilima adasankha ndi ofunikira pofuna kutukula dziko lino.

Exit mobile version