Thursday , July 9 2020
Home / Featured / Peter Kuwani Afunira Zabwino Chakwera ndi Chilima

Peter Kuwani Afunira Zabwino Chakwera ndi Chilima

Mtsogoleri wa Mbakuwaku Movement for Development (MMD) Peter Kuwani omweso amapikisana nawo pa masankho am’tsogoleri wadziko akuti iwo akufunira zabwino mtsogoleri wa Malawi Congress Party (MCP) Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wawo Saulos Chilima pomwe zotsatira zosatsimikizika zamasankhowa zikusonyeza kuti apambana.

“Mdziko lino tinali ndi chisankho cha Pulezidenti pa 23 June 2020 potsatira chigamulo cha bwalo la milandu.
Posalingalira zodandawula zomwe zapelekedwa ku bungwe la chisankho, ine ngati mmodzi mwa omwe timapikisana pa mpando wa Pulezidenti ndikupeleka mafuno abwino kwa Dr. Lazaras Chakwera, wachiwiri wawo (Dr. Saulosi Klaus Chilima) ndi ena onse otsatira Tonse Alliance,”

“Ngakhale zotsatira zomvomelezeka zisadatuluke, komatu manambala sanama.Mwatitchaya dala ndipo ine ngati mtsogoleri wa chipani cha MMD ndimakhulupirira demokalase komaso kulemekeza malamulo,” atero bambo Kuwani.

Bambo Kuwani akuti kudandaula ku bwalo la milandu ngati momwe adachitira ndi ufulu wa m’malawi aliyese ndipo iwo apempha atsogoleri awiriya kuti atukule chuma chadziko lino.

“Upeleka madando siwuchimo chifukwatu mwana ali mchikuta lerori wabadwa chifukwa chamadando.Ngakhale uluza ndichinthu chowawa komatu chosangalatsa mchakuti demokalase ndiyomwe yapambana. Tikukufunilani moyo wathanzi komaso wachisangalalo. Mukapititsa patsogolo ntchito za chuma komaso chitukuko ndiye kuti tonse tapambana ndipo tidzakhala abwezi mpaka muyaya,”

“Mukachita bwino ife tidzawomba mmanja ndipo mukakephela kukwanilitsa malonjezano ife tidzakukwenyani.
Lero mwamwetulira ndipo mawa nafe tidzamwemwetera. Tiyeni tibwezeletse mtendele omwe ndimaziko achuma komaso chitukuko mdziko. Mwana wa mzako akachita koma uyamika,” iwo atero.

About Bright Malenga

Bright Malenga is a Malawian young Media and Communications ethusiast. He is currently pursuing Bachelor of Science in Mass Communication (BSc MAC) at Islamic University in Uganda (IUIU).

Check Also

Nominees to Be Consulted Before Appointment – Chakwera

State President Dr Lazarus Chakwera says the nominated people for his cabinet will be consulted …

%d bloggers like this: