Azimayi achisilamu agulu la Taqwa Taalim Muslim Sisters Organization m’boma la Lilongwe apempha akayidi omwe ali pa ndende ya Maula m’bomali kuti adzilimbikila kupemphera komaso kupanga zinthu zonse zomusangalatsa Allah.
Polankhula ndi Muslim Media Agency dzulo pomwe adakayendela ndende ya Maula, N’kulu wa Bungweli a Rabia Rajab ati kukhala kundende simepeto anzonse.
“Tili kuno ku Maula kufuna kuwalimbitsa mtima azibale athu achisaluma amene ali kuno kuti asataye m’tika sadataike. Iwowo, ndi anthu komaso ansilamu abwino ndipo adzikonda kupemphera komaso kupanga zinthu zomusangalatsa Allah,” Mayi Rajab adatelo.
Malingana ndi wankulu wa Taqwa Taalim Muslim Sisters Organization, ansilamu omwe Ali ku ndendewa akuyenela akhale ndi chiphulupiliro kuti tsiku lina adzakhalaso afulu.
“Kukhala kwao kuno akuyenela kukugwilitsa ntchito bwino pomaswali kasanu patsiku, kulimbikila ma Ibaadah osiyana siyana munyengo in ya Ramadhan popeza kuti apezeke kuno ndi chifunilo cha Allah,” adatero.
Malingana ndi Mayi Rajab, si onse omwe ali kundende oti ndi olakwa popeleka chitsanzo cha Mtumiki Yusuf (AS) yemwe adanamizilidwa kuti wagwilirira n’kazi wa mfumu ndipo adamangidwa.
“M’neneli Yusuf (AS) adanamizilidwa koma kenako ali ku ndende adalimbikila kupanga Ibaadah ndipo adalowetsa Chisilamu anthu ambili kundendeko. Abale athuwaso, kuno ku Maula alimbikile kupanga zabwino zomwe zingakhale muuni kwa anthu omwe sali ansilamu kuona ubwino wa chisilamu,” adatero Mayi Rajab.
Pomalizira, bungwe la azimayiri lidapeleka zakudya zofutulira komaso katundu wina wambili kwa akayidi achisilamu oposa 200 pa ndende ya Maula. Malingana ndi azimayiwa, katundu yemwe adapelekayi athandizila asilamuwa kupanga ma Ibaadah awo munthawi ino ya mwezi wa Ramadhan.