Wapampando wa bungwe la Muslim Association of Malawi (MAM) Sheikh Idrissa Muhammad wapempha asilamu onse mdziko muno kuti ayambe kuthandiza bungweli.
Sheikh Muhammad amalankhula izi pamsonkhano wa atolankhani womwe anachititsa lero mumzinda wa Blantyre.
Mtsogoleri wa asilamuyu wati ndizomvetsa chisoni kuti pali kagulu kena ka asilamu komwe kakumangonena zoyipa za MAM, kunena kuti akuluakulu abungweli akusakaza ndalama chikhalirenicho sanasonkheko ndalama iliyonse.
Iwo anati poyerekeza ndi mabungwe ena oti si asilamu, MAM imadalira thandizo lake kuchokera kwa mabungwe akunja kwa dziko lino ndipo ndalama zake zimakhala ndi ntchito zake kale.
“Asilamu tisinthe maganizidwe athu. Tisamangokamba zoipa za bungwe, kulikakamiza kuti lipange zinthu zoti silingakwanitse kumakhala kuti palibe chomwe timapereka ku bungweli. Kodi ndi ndani ananena kuti poti ndife asilamu ndiye tizingolandira za ulere koma kupereka ayi popeza kuti Chipembedzo chachisilamu ndiye chimalimbikitsa kuperekako? Tangoganizani nthawi ya Qurban munthu kumachoka kutali ngati ku Lilongwe, kuthira mafuta muchigalimoto chodhula kubwera ku Blantyre kukalandira Mbuzi imodzi? Ndalama mwagula mafuta sangakwanitse kugula Mbuzi olo imodzi zoona? Izi sizoona ayi,” atero mtsogoleriyu.
Sheikh Muhammad anawonjezerapo kunena kuti pamene amatenga mpandowu zaka khumi zapitazo analamula atsogoleri amadera onse mdziko muno kuti atsegule ma akaunti akubanki ndi cholinga choti asilamu ayambe kusonkha ndipo kuti ndalamayo izigwiritsidwa popangira zitukuko zing’onozing’ono za deralo.
“Kutha kumva chisoni kumva kuti chitsegulireni akauntiyi sikunaloweko olo ndalama iliyonse mpaka abanki anatseka ma akaunti. Koma lero akubwera ndikumandinyoza ine kuti ndikuba ndalama za asilamu mdziko muno. Ndalama zake ziti popeza simunaperekeko ndalama iliyonse?” Anafunsa motero Sheikh Muhammad.
Mtsogoleriyu anapitilizanso kunena kuti kwa amene ali ndi umboni okwanira woti iwo akusakaza ndalama za asilamu apite ndi umboni ku polisi yomwe ali nayo pafupi kukang’amala.
“Akanene kuti Sheikh Idrissa Muhammad analandira ndalama izi za asilamu komwe ntchito yake sanagwiritse ndipo umboni wake ndi uwu mmalo momangolankhulalankhula mmasamba amchezo,” atero mtsogoleri wa asilamuyu.
Iye anati sakuletsa aliyense kupereka madandaulo ake ku bungweli, kunena kuti khomo ndi lotsegula.
“Atha kuyamba kuwapeza atsogoleri amadela akukhala omwe adzatenge nkhawazo kupititsa kulikulu. Sindinganene kuti ndine mNgelo wosalakwa. Ndili ndi zofooka zanga koma tiyeni titsatire njira yoyenera osati kundiopsyeza kuti mundipha. Mundipha chifukwa chani?” Anadandaula motero Sheikh Idrissa Muhammad.