Nduna m’boma la Tonse a Patricia Kaliati alimbikitsa atsikana mdziko lino kuli adzilimbikira maphunziro awo.
Polemba patsamba lawo la Facebook, a Kaliati ati atsikana omwe amafuna otsogola ndi omwe amapita ku sukulu.
“Mtsikana wanzeru amapita ku school. Atsikana anzanga, anthu awa mukuwaonawa anapita ku school ndipa alimmaudindo osiyanasiyana,” atero a Kaliati.
Iwo alimbikitsa atsikana a kumuzi kuti asimazionele pansi pankhani maphunziro.
“Munthu amachoka patali kwambiri, enafe taphunzira ma school akumudzi ndipo zovuta zinalipo zambiri koma tinapilira, chonde atsikana anzanga kumudziko limbikirani mudzakhale ngati ife,” yatero nduna yabomayi.
Iwo auza atsikana mdziko lino kuti akaneneze aliyese ku polisi ngati akuwasokoneza ngati kuwakakamiza m’banja.
“Ngati wina akukusokonezani chonde, kaneneni ku police, kwamfumu komanso kwina konse komwe mukudziwa kuti atha kukuthandizani.. Sukulu ndinjira yokhayo yomwe ingakupatseni mpata ofika patali,” atero a Kaliyati.
Mawu a Kaliati adza panthawi yomwe atsikana ambiri mdziko lamalawi akusiira sukulu panjira chifukwa chakukwatira adakali achichepele kapena kupatsidwa mimba.