Atoht Manje Atsogolera Asilamu Pomanga Mzikiti

Oyimba Atoht Manje amene dzina lake leni leni ndi Elias Missi yemweso ndi nsilamu watsogolera asilamu pomanga mzikiti pokhotela popita ku Katete mumzinda wa Lilongwe. Oyimbayi wapanga izi popempha anthu ofuna kwabwino kuti akwanilitse maso mphenyawa.

“Some months ago ndimapanga fundraising ya mzikiti uwu. Alemekezeke Mulungu kuti ma contributions a anthu pa page ino ndi ena a mmudzi amene timawapempha thandizo mzikiti mpaka unafika pa roofing level. Kwatsala nkukhoma malata kenako ma finishing,” Watelo Manje.

Manje wafunila zabwino anthuwa onse amene atenga nawo mbali pantchito wabwino.

“Mulungu akudalitseni. Ndinasiya kutolera zopeleka zanu chifukwa tinapeza abale ena amene anazithemba kuti amaliza okha. Alemekeze Mulungu ndipo Mulungu achite nawo mwapadela.Zikomo mpaka nthawi ina tidzabweranso akazamaliza amene atengawo kuti nanu mudzaone pomwe munadzala khobili lanu. Mulungu akudalitseni nonse zikomo,” Manje watero.

Exit mobile version